Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:14 - Buku Lopatulika

14 Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Inu Mulungu wanga, mundikumbukire ine pa zimenezi. Musaiŵale ntchito zanga zabwino zimene ndachitira Nyumba ya Mulungu wanga pofuna kumtumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zimenezi, ndipo musafafanize ntchito zanga zimene ndachita mokhulupirika pa Nyumba yanu pofuna kukutumikirani.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:14
14 Mawu Ofanana  

Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.


Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;


Ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.


Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zochokera kunyumba ya chuma cha mfumu.


Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, antchito a m'kachisi, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira.


Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu,


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.


Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa.


Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa