Nehemiya 13:15 - Buku Lopatulika15 Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Nthaŵi imeneyo ndidaona anthu m'dziko la Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la sabata. Ena ankaunjika tirigu milumilu, nkumasenzetsa abulu. Enanso ankatenga vinyo, mphesa, nkhuyu, ndiponso katundu wa mtundu uliwonse, nkumabwera naye ku Yerusalemu, pa tsiku la sabata. Tsono ndidaŵachenjeza kuti asamagulitse chakudya pa tsiku la sabata. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Nthawi imeneyo ndinaona anthu a mu Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la Sabata. Ena ankawunjika tirigu milumilu ndi kumasenzetsa abulu. Enanso ankabwera ndi vinyo, mphesa, mkuyu ndi katundu wa mitundumitundu ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata. Choncho ndinawachenjeza za kugulitsa zakudya pa tsiku la Sabata. Onani mutuwo |