16 Nawonso anthu ena a ku Tiro okhala mu Yerusalemu, ankabwera ndi nsomba ndi zamalonda za mtundu uliwonse, nkumazigulitsa pa tsiku la sabata kwa anthu a m'dziko la Yuda ndiponso kwa anthu okhala mu mzinda wa Yerusalemu.
16 Nawonso anthu a ku Turo amene ankakhala mu Yerusalemu ankabweretsa nsomba ndi akatundu ena onse amalonda kudzagulitsa pa Sabata kwa anthu a mʼdziko la Yuda ndi a mu Yerusalemu.
Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.