Nehemiya 13:13 - Buku Lopatulika13 Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndinaikanso osunga chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Ndipo ndidasankha aŵa kuti akhale asungachuma: wansembe Selemiya, mlembi Zadoki ndiponso Pedaya mmodzi mwa Alevi, kudzanso mthandizi wao Hanani, mwana wa Zakuri, mdzukulu wa Mataniya, popeza kuti ndidaadziŵa kuti anthuwo anali okhulupirika. Ntchito yao inali yogaŵira abale ao zinthu zofunika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ndipo ndinasankha wansembe Selemiya, mlembi Zadoki, ndi Mlevi wotchedwa Pedaya kukhala oyangʼanira zipinda zosungiramo. Ndinasankhanso Hanani mwana wa Zakuri mwana wa Mataniya kukhala wowathandizira chifukwa ndinaona kuti anthu awa anali odalirika. Ntchito yawo inali yogawira abale awo zinthu zofunika. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.