Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:12 - Buku Lopatulika

12 Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nditachita zimenezi, Ayuda adayambanso kubwera ndi zopereka za chachikhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta, kuti azipereka ku nyumba zosungira chuma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:12
9 Mawu Ofanana  

Anauzanso anthu okhala mu Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'chilamulo cha Yehova.


Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.


Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako.


Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.


Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa