Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
1 Samueli 24:2 - Buku Lopatulika Tsono Saulo anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisraele onse, namuka, kukafuna Davide ndi anthu ake m'matanthwe a zinkhoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsono Saulo anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisraele onse, namuka, kukafuna Davide ndi anthu ake m'matanthwe a zinkhoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adatenga ankhondo okhoza zedi 3,000 amene adaŵasankha pakati pa ankhondo onse. Adapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale. |
Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.
Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.
Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa.
Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m'chipululu cha Zifi.