Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:2 - Buku Lopatulika

2 Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:2
24 Mawu Ofanana  

Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.


Mutipatse ana ake aamuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova mu Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka.


Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini;


Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri.


Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi midzi yake,


ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao.


Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao.


Koma mbuye wake ananena naye, Tisapatukire mzinda wachilendo, wosati wa ana a Israele, koma tipitirire kunka ku Gibea.


Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.


Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;


Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafike masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;


Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.


Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.


Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi.


Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.


Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri.


Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba.


Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.


Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo.


Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo.


Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m'chipululu cha Zifi.


Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa