1 Samueli 13:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. Onani mutuwo |
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku Chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku Chipata cha Kungodya, ndi kuyambira Nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.