1 Samueli 13:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.” Onani mutuwo |
Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu.