Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 13:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:2
24 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti, “Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide, tilibe gawo mwa mwana wa Yese! Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!”


mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”


Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,


Anthu aamuna a ku Mikimasi 122


Nazonso zidzukulu za Benjamini zinkakhala mʼdera lawo kuyambira ku Geba mpaka ku Mikimasi, Ayiya, Beteli ndi midzi yake,


Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.


Ndipo Yoswa anawadalitsa ndi kuwalola kuti apite ndipo anapitadi ku nyumba zawo.


Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.”


Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima.


“Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera.


Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42.


Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?” Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi,


Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600.


Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi.


Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.


Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni.


Tsiku limenelo Aisraeli anapha Afilisti kuchokera ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraeliwo analefuka kwambiri ndi njala.


Thanthwe limodzi linali chakumpoto kuyangʼanana ndi Mikimasi, ndipo thanthwe linalo linali chakummwera kuyangʼanana ndi Geba.


Pa moyo wake wonse, Sauli ankakhalira kuchita nkhondo pakati pa Israeli ndi Afilisti. Ndipo Sauli ankati akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima ankamulemba ntchito mu gulu lake lankhondo.


Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli.


Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo.


Choncho Sauli ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake 3,000 napita ku chipululu cha Zifi kukafunafuna Davide ku chipululuko.


Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa