Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
1 Samueli 22:8 - Buku Lopatulika kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.” |
Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani?
Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.
Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha.
Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.
Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe?