1 Samueli 22:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Saulo adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wandichita chiwembu iwe ndi mwana wa Yese? Wampatsa buledi ndi lupanga, ndipo wamfunsira kwa Mulungu zoti achite. Taonani, tsopano wandiwukira, ndipo akundilalira lero lino!” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Sauli anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ndi mwana wa Yese mwandiwukira ine? Wamupatsa buledi ndi lupanga. Wafunsiranso kwa Yehova zoti andiwukire ndi kundibisalira monga wachita leromu?” Onani mutuwo |