Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.
1 Samueli 22:1 - Buku Lopatulika Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Davide adathaŵa ku Gati, nakabisala ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi onse a m'banja la bambo wake atamva, adapita kumene kunali Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anachoka kumeneko nathawira ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi banja lonse la abambo ake anamva izi, anapita kumene kunali Davide. |
Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.
Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu.
Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.
Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu.
Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m'malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.
(amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.