Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 11:38 - Buku Lopatulika

38 (amenewo dziko lapansi silinayenere iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Anthu ameneŵa, pansi pano sipadaŵayenere! Ankangoyenda m'zipululu ndi m'mapiri namabisala m'mapanga ndi m'maenje apansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 11:38
16 Mawu Ofanana  

Choka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani.


Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanu asanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi?


pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.


Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?


Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza.


Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.


Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.


Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.


Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi.


Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu?


Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda.


Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa