ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
1 Samueli 21:12 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mau ameneŵa Davide adamloŵa mu mtima kwambiri, ndipo adayamba kuwopa Akisi mfumu ya ku Gati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu amenewa anamulowa kwambiri Davide mu mtima ndipo anayamba kuopa kwambiri Akisi mfumu ya ku Gati. |
ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.
Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.
Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.
Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.
Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake.