Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 2:19 - Buku Lopatulika

19 Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira.

Onani mutuwo Koperani




Luka 2:19
10 Mawu Ofanana  

Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.


Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.


Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga.


Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo.


Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.


Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao.


Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.


Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa