1 Samueli 21:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Tsono nduna za Akisi zidamufunsa Akisiyo kuti, “Kodi ameneyu si Davide, mfumu ya dziko? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankamuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi, inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, “Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti, “Sauli wapha 1,000, koma Davide wapha miyandamiyanda?” Onani mutuwo |