1 Samueli 18:9 - Buku Lopatulika Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwake, Saulo anakhala maso pa Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwake, Saulo anakhala maso pa Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Saulo ankamuwona ndi diso loipa Davide kuyambira tsiku limenelo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide. |
Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino?
zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:
Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.
Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo.
Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha?
Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.