1 Samueli 18:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake. Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.