Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.
1 Samueli 18:6 - Buku Lopatulika Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m'mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anatuluka m'midzi yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene anthu ankabwerera kwao, Davide atapha Mfilisti uja, akazi adatuluka m'mizinda yonse ya Aisraele akuimba ndi kuvina, kuti achingamire mfumu Saulo. Ankaimba ndi kumavina mokondwa, kwinaku ng'oma ndi zitoliro zikugundika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira. |
Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.
Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje.
Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja.
Ndipo nthawi zonse Yehova adzawakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyanathunyana, Iye adzamenyana nao.
Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.
Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.