Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 68:25 - Buku Lopatulika

25 Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola, oimba ndi zipangizo ali pambuyo, anamwali oimba ting'oma ali pakati.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo; pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:25
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.


Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani.


Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.


Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati, akasupe anga onse ali mwa inu.


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao.


Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.


Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi.


Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m'mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa