Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:11 - Buku Lopatulika

11 Ambuye anapatsa mau, akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ambuye anapatsa mau, akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ambuye analengeza mawu, ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:11
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.


Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;


Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu.


Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?


Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu aakazi anatuluka m'mizinda yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa