Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:12 - Buku Lopatulika

12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro; mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:12
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito.


nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse.


Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova.


Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda.


Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.


Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;


Anadza mafumu nathira nkhondo; pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani. Mu Taanaki, ku madzi a Megido; osatengako phindu la ndalama.


Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.


Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa