Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
1 Samueli 13:11 - Buku Lopatulika Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafike masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele adamufunsa Sauloyo kuti, “Nanga nchiyaninso mwachitachi?” Iye adayankha kuti, “Pamene ndinaona kuti anthu akundithaŵira, ndipo kuti inuyo nthaŵi imene mudaanena ija simudabwere, ndiponso kuti Afilisti adasonkhana ku Mikimasi, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?” Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, |
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi.
Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?
Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.
chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.
Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.
Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.
Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba.