Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 13:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono iyeyo ndi mwana wake Yonatani, pamodzi ndi anthu amene anali nawowo, adakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti adamanga zithando zankhondo ku Mikimasi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 13:16
4 Mawu Ofanana  

wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibea wa Saulo wathawa.


Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.


Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.


Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa