1 Samueli 1:5 - Buku Lopatulika koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ngakhale ankakonda Hana, ankangompatsa gawo limodzi chifukwa choti Chauta sadampatse ana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. |
Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara.
Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.
Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.
Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba?
Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.
Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu.
Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;