1 Samueli 1:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tsiku limene Elikana ankapereka nsembe, ankapatsako magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake aamuna ndi aakazi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. Onani mutuwo |
Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu aamuna, ndi ana anu aakazi, ndi antchito anu aamuna, ndi antchito anu aakazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.