Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:1 - Buku Lopatulika

1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Rakele ataona kuti sakumubalira ana Yakobe, adayamba kuchita nsanje ndi mkulu wake uja, ndipo adauza Yakobe kuti, “Mundipatse ana, apo ai, ndingofa basi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Rakele ataona kuti sakumuberekera Yakobo ana, anayamba kumuchitira nsanje mʼbale wake. Choncho anati kwa Yakobo, “Undipatse ana kapena apo ayi ndingofa!”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:1
26 Mawu Ofanana  

Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.


Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake.


Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.


Ndaniyo adzatsutsana nane? Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga.


Ndinalekeranji kufera m'mimba? Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine.


Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova.


Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.


Manda, ndi chumba, dziko losakhuta madzi, ndi moto wosanena, Kwatha.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.


Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!


anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya.


Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumzinda kuti akagule chakudya.


pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?


Pakuti chisoni cha kwa Mulungu chitembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa.


njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa