Davide aimbira ulemerero wa Mulungu, ndi ulemu umene Mulungu achitira mtundu wa anthuKwa Mkulu wa Nyimbo: pa Gititi. Salimo la Davide. 1 Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba. 2 M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango. 3 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, 4 munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? 5 Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu. 6 Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; 7 nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama zakuthengo zomwe; 8 mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja. 9 Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi