Pemphero pakuopsedwa kwakukuluChilangizo cha Davide, muja anakhala m'phanga; Pemphero. 1 Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova; ndi mau anga ndipemba kwa Yehova. 2 Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake. 3 Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha. 4 Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga. 5 Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo. 6 Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana. 7 Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi