Yoweli 3:7 - Buku Lopatulika taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ndidzaŵadzutsa kuti achoke kumalo kumene mudaŵagulitsa. Kenaka ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu. |
Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi.
Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani.
Mau a phokoso achokera m'mzinda, mau ochokera mu Kachisi, mau a Yehova amene abwezera adani ake chilango.
koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m'dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.
Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.
Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusiridwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.
Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.
Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu.
Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.
Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Filistiya? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu.
Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi.
Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.
Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.
Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.