Oweruza 1:7 - Buku Lopatulika7 Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Apo Adonibezeki adati, “Mafumu makumi asanu ndi aŵiri oduka zala zazikulu zakumanja ndi zakumwendo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu wandichita zomwe ndidaŵachita iwowo.” Anthu ake adapita naye ku Yerusalemu ndipo iye adafera komweko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko. Onani mutuwo |
Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake aamuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo paguwa la nsembe posungulira.