Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Yoweli 2:7 - Buku Lopatulika Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m'mabande ao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m'mabande ao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akududuka ngati ankhondo. Akukwera malinga ngati asilikali. Aliyense akuyenda pa mzere, osasempha njira yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amathamanga ngati ankhondo; amakwera makoma ngati asilikali. Onse amayenda pa mizere, osaphonya njira yawo. |
Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.
Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.
ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake, likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira.
Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.