Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.
Yoweli 1:5 - Buku Lopatulika Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire. Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo: mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire! Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo; lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano, pakuti wachotsedwa pakamwa panu. |
Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerere pa ife.
Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika.
Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.
Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.
Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;