Yoweli 1:6 - Buku Lopatulika6 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano a chibwano a mkango waukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano achibwano a mkango waukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Chikhamu cha dzombe chagwa m'dziko lathu nchamphamvu ndiponso chosaŵerengeka. Mano ake ali ngati a mkango wamphongo, zibwano zake ngati za mkango waukazi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa, wamphamvu ndi wosawerengeka; uli ndi mano a mkango, zibwano za mkango waukazi. Onani mutuwo |