Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 1:4 - Buku Lopatulika

4 Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Chimene chiwala chidasiya, dzombe lidadya. Chimene dzombe lidasiya, mandowa adadya, chimene mandowa adasiya, chilimamine adadya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Chimene dzombe losamera mapiko lasiya dzombe lowuluka ladya; chimene dzombe lowuluka lasiya dzombe lalingʼono ladya; chimene dzombe lalingʼono lasiya chilimamine wadya.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 1:4
19 Mawu Ofanana  

M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;


Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;


Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga;


Ananena, ndipo linadza dzombe ndi mphuchi, ndizo zosawerengeka,


Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao, ndi dzombe ntchito yao.


pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;


ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo;


Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.


Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu.


Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.


Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu.


Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.


Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.


Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa