Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Numeri 9:18 - Buku Lopatulika Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa chihema amakhala m'chigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa Kachisi amakhala m'chigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula, ndipo ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula. Nthaŵi yonse pamene mtambowo unali pa chihemacho, iwo ankakhalabe m'mahema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo. |
Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.
Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.
Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;
Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.