Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa chihema masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa Kachisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:20
8 Mawu Ofanana  

Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.


Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako;


umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.


Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.


Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa chihema amakhala m'chigono.


Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa chihema, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.


Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo.


Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa