Ndipo m'chipinda chamkatimo anasema mitengo ya azitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.
Numeri 7:89 - Buku Lopatulika Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ataloŵa m'chihema chamsonkhano kukalankhula ndi Chauta, adamva mau kuchokera pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi laumboni, pakati pa akerubi. Mulungu adalankhula naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye. |
Ndipo m'chipinda chamkatimo anasema mitengo ya azitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke.
Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.
Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.
Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.
Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.