Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 40:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Mose sadathe kuloŵa m'chihema chamsonkhanocho chifukwa mtambo unali momwemo, ndipo ulemerero wa Chauta udaadzaza chihema chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 40:35
15 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova.


Ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.


Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.


Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anafuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova.


Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa mu Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum'mawa.


ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.


Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye.


Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.


Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa mu Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa