Numeri 7:88 - Buku Lopatulika88 ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201488 ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa88 Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero88 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa. Onani mutuwo |