Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 7:88 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

88 Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

88 ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

88 ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

88 Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 7:88
5 Mawu Ofanana  

Pa nsembe yachiyanjanopo ayenera kuchotsa ndi kubweretsa: mafuta a nkhosayo, mchira wake wonse wonona atawudulira mʼtsinde pafupi ndi fupa la msana, zamʼkati zonse ndi mafuta onse amene akuta ziwalo zamʼkatimo,


Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse.


Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo.


Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri.


Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa