Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 5:9 - Buku Lopatulika

Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zopereka zonse zopatulika za Aisraele zimene amabwera nazo kwa wansembe, zikhale zake za wansembe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zopereka zonse zopatulika zomwe Aisraeli abwera nazo kwa wansembe zikhale za wansembeyo.

Onani mutuwo



Numeri 5:9
19 Mawu Ofanana  

ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.


ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero.


Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.


Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nao pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako aamuna, mwa lemba losatha; monga Yehova analamula.


Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.


Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe ukhale nsembe yokweza yochokera ku nsembe zoyamika zanu.


Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.


Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.


Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.


Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.


Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;