Levitiko 10:14 - Buku Lopatulika14 Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Koma nganga yopereka moweyula manja ija, pamodzi ndi ntchafu yopereka, muzidyere pa malo aliwonse oyenera pa zachipembedzo, iweyo ndi ana ako aamuna ndi aakazi amene ali nawe. Zimenezi zapatsidwa kwa iwe kuti zikhale zako ndi za ana ako, kuchokera pa nsembe yachiyanjano imene aipereka Aisraele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Koma iwe pamodzi ndi ana ako aamuna ndi aakazi muzidya chidale chimene chinaweyulidwa ndi ntchafu zimene zinaperekedwa nsembe. Muzidye pamalo woyeretsedwa. Zimenezi zaperekedwa kwa iwe ndi ana ako monga gawo lanu pa zopereka zachiyanjano zimene apereka Aisraeli. Onani mutuwo |
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.