Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 31:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Mose adapereka kwa wansembe Eleazara gawo limene linali loyenera kulipereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Moseyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Mose anapereka kwa wansembe Eliezara gawo limene linali loyenera kupereka kwa Yehova monga momwe Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:41
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.


Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.


Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri.


Ndipo kunena za gawo la ana a Israele, limene Mose adalichotsa kwa anthu ochita nkhondowo,


Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zisanduka zake.


Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.


kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.


Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino.


Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa