Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 7:34 - Buku Lopatulika

34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Choncho nganga yopereka moweyula manjayo, pamodzi ndi ntchafu yoperekayo, ndikuzichotsa zonsezo kwa Aisraele. Ndikuzichotsa pa nsembe zao zachiyanjano, ndipo ndikuzipereka kwa wansembeyo Aroni ndi kwa ana ake, kuti zikhale chigawo chao nthaŵi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:34
12 Mawu Ofanana  

Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.


Uwamangirenso Aroni ndi ana ake aamuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake aamuna.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.


Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.


ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.


ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova.


Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa