Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 29:28 - Buku Lopatulika

28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Pa zimene Aisraele azipereka, zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake nthaŵi zonse. Alandire ndiwo ansembe zonsezi zochokera pa zopereka zamtendere za Aisraele pakuti ndizo mphatso zao za Aisraele kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:28
18 Mawu Ofanana  

Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma.


Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake aamuna;


Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala;


Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.


Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu.


Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele.


Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.


Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.


Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.


Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose.


Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zisanduka zake.


Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.


ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.


Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa