13 Muzidye pa malo oyera, chifukwa zimenezi ndakugaŵiraniko kuchokera pa nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta, kuti zikhale zanu, iwe ndi ana ako. Ndithudi, zimenezi ndizo zimene Chauta adandilamula.
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.
Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;
Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako aamuna, ndi ana ako aakazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako aamuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele.