Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 5:23 - Buku Lopatulika

Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Wansembe alembe m'buku matemberero ameneŵa ndipo aŵafafanize poŵaviika m'madzi oŵaŵa aja.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“ ‘Wansembe alembe matemberero amenewa mʼbuku ndi kuwanyika mʼmadzi owawa aja.

Onani mutuwo



Numeri 5:23
14 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo choipa, ndicho matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;


Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera, chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe; mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wanga!


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.


Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.


Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;


Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israele iyi; muiike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indichitire mboni yotsutsa ana a Israele.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.