Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 5:22 - Buku Lopatulika

22 ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Madzi ali apa amatembereroŵa aloŵe m'matumbo mwako, atupitse thupi lako, ndipo afwapitse m'chiwuno mwako.’ Tsono mkaziyo avomere kuti, ‘Inde momwemo! Inde momwemo!’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Madzi awa obweretsa temberero alowe mʼthupi mwako ndi kutupitsa mimba yako ndi kuwononga ntchafu yako.’ ” “Pamenepo mkaziyo anene kuti, ‘Ameni, ameni.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 5:22
16 Mawu Ofanana  

Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake.


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.


Wodalitsika Yehova kunthawi yonse. Amen ndi Amen.


momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao.


Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi.


Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.


Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake.


Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa